Masalimo 6 - The Word of God in Contemporary Chichewa

Salimo 6Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Molingana ndi seminiti. Salimo la Davide.

1Inu Yehova, musandidzudzule mu mkwiyo wanu,

kapena kundilanga mu ukali wanu.

2Ndichitireni chifundo Inu Yehova, pakuti ndalefuka;

Inu Yehova chiritseni, pakuti mafupa anga ali pa ululu waukulu.

3Moyo wanga uli pa mazunzo aakulu.

Mpaka liti, Inu Yehova, mpaka liti?

4Tembenukani Inu Yehova, ndipo mundilanditse;

pulumutseni chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika.

5Palibe amene amakukumbukirani pamene wamwalira;

Amakutamandani ndani ali ku manda?

6Ine ndatopa ndi kubuwula;

usiku wonse pa bedi panga pamadzaza ndi misozi yanga;

ndimanyowetsa pogona panga ndi misozi.

7Maso anga atupa chifukwa cha chisoni;

akulephera kuona chifukwa cha adani anga.

8Chokani kwa ine inu nonse amene mumachita zoyipa,

pakuti Yehova wamva kulira kwanga.

9Yehova wamva kupempha kwanga kofuna chifundo;

Yehova walandira pemphero langa.

10Adani anga onse adzachita manyazi ndipo adzakhala ndi mantha;

adzabwerera msangamsanga mwa manyazi.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help