Masalimo 114 - The Word of God in Contemporary Chichewa

Salimo 114

1Pamene Israeli anatuluka mu Igupto,

nyumba ya Yakobo kuchoka ku mtundu wa anthu a chiyankhulo chachilendo,

2Yuda anasanduka malo opatulika a Mulungu,

Israeli anasanduka ufumu wake.

3Nyanja inaona ndi kuthawa,

mtsinje wa Yorodani unabwerera mʼmbuyo;

4mapiri analumphalumpha ngati nkhosa zazimuna,

timapiri ngati ana ankhosa.

5Nʼchifukwa chiyani iwe unathawa?

iwe mtsinje wa Yorodani unabwereranji mʼmbuyo?

6inu mapiri, munalumphalumphiranji ngati nkhosa zazimuna,

inu timapiri, ngati ana ankhosa?

7Njenjemera pamaso pa Ambuye iwe dziko lapansi,

pamaso pa Mulungu wa Yakobo,

8amene anasandutsa thanthwe kukhala chitsime,

thanthwe lolimba kukhala akasupe a madzi.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help