Masalimo 123 - The Word of God in Contemporary Chichewa

Salimo 123Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

1Ndikweza maso anga kwa Inu,

kwa Inu amene mumakhala kumwamba.

2Taonani, monga momwe maso a akapolo amayangʼana mʼdzanja la mbuye wawo,

monga momwenso maso a mdzakazi amayangʼana mʼdzanja la dona wake,

choncho maso athu ali kwa Yehova Mulungu wathu,

mpaka atichitire chifundo.

3Mutichitire chifundo, Inu Yehova mutichitire chifundo,

pakuti tapirira chitonzo chachikulu.

4Ife tapirira mnyozo wambiri kuchokera kwa anthu odzikuza,

chitonzo chachikulu kuchokera kwa anthu onyada.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help