Masalimo 64 - The Word of God in Contemporary Chichewa

Salimo 64Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

1Ndimvereni Mulungu pomwe ndikunena madandawulo anga;

tetezani moyo wanga ku chiopsezo cha mdani.

2Ndibiseni ku chiwembu cha anthu oyipa,

ku gulu laphokoso la anthu ochita zoyipa.

3Iwo amanola malilime awo ngati malupanga,

amaponya mawu awo olasa ngati mivi.

4Iwo amaponya mivi yawo ali pa malo wobisala kwa munthu wosalakwa;

amamulasa modzidzimutsa ndi mopanda mantha.

5Iwo amalimbikitsana wina ndi mnzake pa chikonzero chawo choyipa,

amayankhula zobisa misampha yawo;

ndipo amati, “Adzayiona ndani?”

6Iwo amakonzekera zosalungama ndipo amati,

“Takonza ndondomeko yabwino kwambiri!”

Ndithu maganizo ndi mtima wa munthu ndi zachinyengo.

7Koma Mulungu adzawalasa ndi mivi;

mwadzidzidzi adzakanthidwa.

8Iye adzatembenuza milomo yawoyo kuwatsutsa

ndi kuwasandutsa bwinja;

onse amene adzawaona adzagwedeza mitu yawo mowanyoza.

9Anthu onse adzachita mantha;

adzalengeza ntchito za Mulungu

ndi kulingalira mozama zomwe Iye wazichita.

10Lolani wolungama akondwere mwa Yehova

ndi kubisala mwa Iye,

owongoka mtima onse atamande Iye!

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help