Masalimo 23 - The Word of God in Contemporary Chichewa

Salimo 23Salimo la Davide.

1Yehova ndiye mʼbusa wanga, sindidzasowa kanthu.

2Amandigoneka pa msipu wobiriwira,

amanditsogolera ku madzi akumwa abwino,

3amatsitsimutsa moyo wanga.

Amanditsogolera mʼnjira zachilungamo

chifukwa cha dzina lake.

4Ngakhale ndiyende

mʼchigwa cha mdima wakuda bii,

sindidzaopa choyipa,

pakuti Inu muli ndi ine;

chibonga chanu ndi ndodo yanu

zimanditonthoza.

5Mumandikonzera chakudya

adani anga akuona.

Mumadzoza mutu wanga ndi mafuta;

chikho changa chimasefukira.

6Zoonadi, zokoma ndi chikondi chosasinthika zidzanditsata

masiku onse a moyo wanga,

ndipo ndidzakhala mʼNyumba ya Yehova

kwamuyaya.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help