Masalimo 126 - The Word of God in Contemporary Chichewa

Salimo 126Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

1Yehova atabwezera akapolo ku Ziyoni,

tinali ngati amene akulota.

2Pakamwa pathu panadzaza ndi kuseka;

malilime athu ndi nyimbo zachimwemwe.

Pamenepo kunanenedwa pakati pa anthu kuti,

“Yehova wawachitira zinthu zazikulu.”

3Yehova watichitira zinthu zazikulu,

ndipo tadzazidwa ndi chimwemwe.

4Tibwezereni madalitso athu, Inu Yehova,

monga mitsinje ya ku Negevi.

5Iwo amene amafesa akulira,

adzakolola akuyimba nyimbo zachimwemwe.

6Iye amene amayendayenda nalira,

atanyamula mbewu yokafesa,

adzabwerera akuyimba nyimbo zachimwemwe,

atanyamula mitolo yake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help