Masalimo 85 - The Word of God in Contemporary Chichewa

Salimo 85Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la ana a Kora.

1Yehova munakomera mtima dziko lanu;

munabwezeretsa ulemerero wa Yakobo.

2Munakhululukira mphulupulu za anthu anu

ndi kuphimba machimo awo onse.

Sela

3Munayika pambali ukali wanu wonse

ndi kutembenuka kuchoka ku mkwiyo wanu woopsa.

4Tibwezeretseninso mwakale Inu Mulungu Mpulumutsi wathu,

ndipo mutichotsere mkwiyo wanu.

5Kodi mudzatikwiyira mpaka liti?

Kodi mudzapitiriza kukwiya pa mibado yathu yonse?

6Kodi simudzatitsitsimutsanso,

kuti anthu anu asangalale mwa Inu?

7Tionetseni chikondi chanu chosatha, Inu Yehova,

ndipo tipatseni chipulumutso chanu.

8Ndidzamvetsera zimene Yehova Mulungu adzanena;

Iye amalonjeza mtendere kwa anthu ake, oyera mtima ake,

koma musawalole kuti abwerere ku zopusa.

9Ndithu chipulumutso chake chili pafupi ndi iwo amene amaopa Iye,

kuti ulemerero wake ukhale mʼdziko lathu.

10Chikondi ndi kukhulupirika zimakumana pamodzi;

chilungamo ndi mtendere zimapsompsonana.

11Kukhulupirika kumatumphuka kuchokera ku dziko lapansi,

ndipo chilungamo chimayangʼana pansi kuchokera kumwamba.

12Ndithu Yehova adzapereka chimene chili chabwino,

ndipo dziko lathu lidzapereka zokolola zake.

13Wolungama amapita patsogolo pake

ndi kukonza njira za mapazi ake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help