Masalimo 4 - The Word of God in Contemporary Chichewa

Salimo 4Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe wa zida za zingwe. Salimo la Davide.

1Ndiyankheni pamene ndiyitana Inu,

Inu Mulungu wa chilungamo changa.

Pumulitseni ku zowawa zanga;

chitireni chifundo ndi kumva pemphero langa.

2Anthu inu, mpaka liti mudzakhala mukusandutsa ulemerero wanga kukhala manyazi?

Mpaka liti mudzakonda zachabe ndi kufuna milungu yabodza?

Sela.

3Dziwani kuti Yehova wadziyikira padera anthu okhulupirika;

Yehova adzamva pamene ndidzamuyitana.

4Kwiyani koma musachimwe;

pamene muli pa mabedi anu,

santhulani mitima yanu ndi kukhala chete.

Sela

5Perekani nsembe zolungama

ndipo dalirani Yehova.

6Ambiri akufunsa kuti, “Ndani angationetse chabwino chilichonse?”

Kuwunika kwa nkhope yanu kutiwalire, Inu Yehova.

7Inu mwadzaza mtima wanga ndi chimwemwe chachikulu

kuposa kuchuluka kwa tirigu wawo ndi vinyo watsopano.

8Ine ndidzagona ndi kupeza tulo mwamtendere,

pakuti Inu nokha, Inu Yehova,

mumandisamalira bwino.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help