1Bwerani, mutamande Yehova, inu atumiki onse a Yehova,
amene mumatumikira usiku mʼnyumba ya Yehova.
2Kwezani manja anu mʼmalo opatulika
ndipo mutamande Yehova.
3Yehova wolenga kumwamba ndi dziko lapansi,
akudalitseni kuchokera mʼZiyoni.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.