Hoseya 5 - The Word of God in Contemporary Chichewa

Chiweruzo cha Israeli

1“Ansembe inu, imvani izi!

Inu Aisraeli, tcherani khutu!

Inu nyumba yaufumu, mvetserani!

Chiweruzo ichi ndi chotsutsa inu:

Inu munali ngati msampha ku Mizipa,

munali ngati ukonde woyalidwa pa phiri la Tabori.

2Owukira azama mʼmoyo wakupha,

Ine ndidzawalanga onsewo.

3Ndimadziwa zonse za Efereimu;

Aisraeli ndi osabisika kwa Ine.

Efereimu wayamba tsopano kuchita zachiwerewere;

Israeli wadziyipitsa.

4“Ntchito zawo siziwalola

kubwerera kwa Mulungu wawo.

Mʼmitima mwawo muli mzimu wachiwerewere;

Iwo sadziwa Yehova.

5Kudzikuza kwa Israeli kwakhala umboni womutsutsa;

Aisraeli, ngakhale Aefereimu, anagwa mʼmachimo awo;

Yudanso anagwa nawo pamodzi.

6Pamene adzapita ndi nkhosa zawo ndi ngʼombe zawo

kukapereka nsembe kwa Yehova,

iwo sadzamupeza;

Iye wawachokera.

7Iwo ndi osakhulupirika kwa Yehova;

amabereka ana amʼchigololo

ndipo chikondwerero chawo cha mwezi watsopano

chidzawawononga pamodzi ndi minda yawo.

8“Womba lipenga mu Gibeya,

liza mbetete mu Rama.

Fuwulani mfuwu wankhondo mu Beti-Aveni;

iwe Benjamini tsogolera.

9Efereimu adzasanduka bwinja

pa tsiku la chilango.

Ine ndikulengeza zomwe zidzachitikadi

pakati pa mafuko a Israeli.

10Atsogoleri a Yuda ali ngati anthu

amene amasuntha miyala ya mʼmalire.

Ndidzawakhutulira ukali wanga

ngati madzi a chigumula.

11Efereimu waponderezedwa,

akulangidwa chifukwa chotsatira

mafano.

12Ine ndili ngati njenjete kwa Efereimu,

ngati chinthu chowola kwa anthu a ku Yuda.

13“Efereimu ataona nthenda yake,

ndi Yuda ataona zilonda zake,

pamenepo Efereimu anatembenukira kwa Asiriya,

ndipo anawatumizira mfumu yayikulu kudzawathandiza.

Koma mfumuyo singathe kukuchizani,

singathe kuchiritsa mabala anu.

14Pakuti Ine ndidzakhala ngati mkango kwa Efereimu.

Ngati mkango wamphamvu kwa Yuda.

Ndidzawakhadzula nʼkuchokapo;

ndidzawatenga ndipo palibe amene adzawalanditse.

15Ndipo ndidzabwerera ku malo anga

mpaka anthu anga atavomereza kulakwa kwawo.

Ndipo iwo adzafunafuna nkhope yanga;

mʼmasautso awo adzandifunitsitsa Ine.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help