Masalimo 12 - The Word of God in Contemporary Chichewa

Salimo 12Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Monga mwa mayimbidwe seminiti. Salimo la Davide.

1Thandizeni Yehova pakuti palibe munthu wokhulupirika;

okhulupirika akusowa pakati pa anthu.

2Aliyense amanamiza mʼbale wake;

ndi pakamwa pawo pabodza amayankhula zachinyengo.

3Inu Yehova tsekani milomo yonse yachinyengo

ndi pakamwa paliponse podzikuza.

4Pakamwa pamene pamati, “Ife tidzapambana ndi kuyankhula kwathu;

pakamwapa ndi pathupathu, tsono mbuye wathu ndani?”

5“Chifukwa cha kuponderezedwa kwa anthu opanda mphamvu

ndi kubuwula kwa anthu osowa,

Ine ndidzauka tsopano,” akutero Yehova,

“Ndidzawateteza kwa owazunza.”

6Ndipo mawu a Yehova ndi angwiro

monga siliva oyengedwa mʼngʼanjo yadothi,

oyengedwa kasanu nʼkawiri.

7Inu Yehova mudzatitchinjiriza ndipo

mudzatiteteza kwa anthu otere kwamuyaya.

8Oyipa amangoyendayenda ponseponse

anthu akamayamikira zochita zawo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help