Masalimo 30 - The Word of God in Contemporary Chichewa

Salimo 30Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba popereka Nyumba ya Mulungu.

1Ndidzakukwezani Yehova,

chifukwa mwanditulutsa kwakuya,

ndipo simunalole kuti adani anga akondwere pa ine.

2Inu Yehova Mulungu wanga ndinapempha kwa Inu thandizo

ndipo Inu munandichiritsa.

3Inu Yehova, munanditulutsa ku manda,

munandisunga kuti ndisatsalire mʼdzenje.

4Imbirani Yehova inu anthu ake okhulupirika;

tamandani dzina lake loyera.

5Pakuti mkwiyo wake umakhala kwa kanthawi

koma kukoma mtima kwake ndi kwa moyo wonse;

utha kuchezera kulira usiku wonse,

koma chimwemwe chimabwera mmawa.

6Pamene ndinaona kuti ndili otetezedwa ndinati,

“Sindidzagwedezekanso.”

7Inu Yehova, pamene munandikomera mtima,

munachititsa phiri langa kuyima chilili;

koma pamene munabisa nkhope yanu,

ndinataya mtima.

8Kwa Inu Yehova ndinayitana;

kwa Ambuye ndinapempha chifundo;

9“Kodi pali phindu lanji powonongeka kwanga

ngati nditsikira ku dzenje?

Kodi fumbi lidzakutamandani Inu?

Kodi lidzalengeza za kukhulupirika kwanu?

10Imvani Yehova ndipo mundichitire chifundo;

Yehova mukhale thandizo langa.”

11Inu munasandutsa kulira kwanga kukhala kuvina;

munachotsa chiguduli changa ndi kundiveka ndi chimwemwe,

12kuti mtima wanga uthe kuyimbira Inu usakhale chete.

Yehova Mulungu wanga, ndidzapereka kwa Inu mayamiko kwamuyaya.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help