Masalimo 14 - The Word of God in Contemporary Chichewa

Salimo 14Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

1Chitsiru chimati mu mtima mwake,

“Kulibe Mulungu.”

Oterewa ndi oyipa ndipo ntchito zawo ndi zonyansa;

palibe amene amachita zabwino.

2Yehova kumwamba wayangʼana pansi,

kuyangʼana anthu onse

kuti aone ngati alipo wina wanzeru,

amene amafunafuna Mulungu.

3Onse atembenukira kumbali,

onse pamodzi asanduka oyipa;

palibe amene amachita zabwino,

palibiretu ndi mmodzi yemwe.

4Kodi anthu ochita zoyipawa sadziwa chilichonse?

Akudya anthu anga ngati chakudya chawo

ndipo satamanda Yehova?

5Awo ali apowo, agwidwa ndi mantha aakulu,

pakuti Mulungu ali mʼgulu la olungama.

6Inu ochita zoyipa mumalepheretsa chikonzero cha anthu osauka,

koma Yehova ndiye pothawirapo pawo.

7Ndithu, chipulumutso cha Israeli chidzachokera ku Ziyoni!

Pamene Yehova abwezeretsa ufulu wa anthu ake,

Yakobo akondwere ndipo Israeli asangalale!

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help