Masalimo 143 - The Word of God in Contemporary Chichewa

Salimo 143Salimo la Davide.

1Yehova imvani pemphero langa,

mvetserani kulira kwanga kopempha chifundo;

mwa kukhulupirika kwanu ndi chilungamo chanu

bwerani kudzandithandiza.

2Musazenge mlandu mtumiki wanu,

pakuti palibe munthu wamoyo amene ndi wolungama pamaso panu.

3Mdani akundithamangitsa,

iye wandipondereza pansi;

wachititsa kuti ndikhale mu mdima

ngati munthu amene anafa kale.

4Choncho mzimu wanga ukufowoka mʼkati mwanga;

mʼkati mwanga, mtima wanga uli ndi nkhawa.

5Ndimakumbukira masiku amakedzana;

ndimalingalira za ntchito yanu yonse,

ndimaganizira zimene manja anu anachita.

6Ndatambalitsa manja anga kwa Inu;

moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Inu monga nthaka yowuma.

Sela

7Yehova ndiyankheni msanga;

mzimu wanga ukufowoka.

Musandibisire nkhope yanu,

mwina ndidzakhala ngati iwo amene atsikira ku dzenje.

8Lolani kuti mmawa ubweretse mawu achikondi chanu chosasinthika,

pakuti ine ndimadalira Inu.

Mundisonyeze njira yoti ndiyendemo,

pakuti kwa Inu nditukulira moyo wanga.

9Pulumutseni kwa adani anga, Inu Yehova,

pakuti ndimabisala mwa Inu.

10Phunzitseni kuchita chifuniro chanu,

popeza ndinu Mulungu wanga;

Mzimu wanu wabwino unditsogolere

pa njira yanu yosalala.

11Sungani moyo wanga Inu Yehova chifukwa cha dzina lanu;

mwa chilungamo chanu tulutseni mʼmasautso anga.

12Mwa chikondi chanu chosasinthika khalitsani chete adani anga;

wonongani adani anga,

pakuti ndine mtumiki wanu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help