1Zakumwamba zimalengeza za ulemerero wa Mulungu;
thambo limalalikira ntchito za manja ake.
2Tsiku ndi tsiku zimayankhula mawu ambiri,
usiku ndi usiku zimaonetsa poyera nzeru.
3Palibe kuyankhula, palibe mawu aliwonse;
liwu lawo silimveka.
4Koma uthenga wawo umapita pa dziko lonse lapansi,
mawuwo amafika mpaka
kumalekezero a dziko lapansi.
5Dzuwa lili ngati mkwatibwi wobwera kuchokera ku nsanja yake,
ngati katswiri wokondwerera kuthamanga pa mpikisano.
6Limatuluka kuyambira mbali ina ya thambo
ndi kuzungulira mpaka mbali inanso;
palibe chinthu chotha kupewa kutentha kwake.
7Lamulo la Yehova ndi langwiro,
kutsitsimutsa moyo.
Maumboni a Yehova ndi odalirika,
amapereka nzeru kwa wopanda nzeru.
8Malangizo a Yehova ndi olungama,
amapereka chimwemwe mu mtima.
Malamulo a Yehova ndi onyezimira,
amapereka kuwala.
9Kuopa Yehova ndiye chinthu changwiro,
chimakhala mpaka muyaya.
Maweruzo a Yehova ndi owona
ndipo onse ndi olungama;
10ndi a mtengowapatali kuposa golide,
kuposa golide weniweni;
ndi otsekemera kuposa uchi,
kuposa uchi wochokera pa chisa chake.
11Mtumiki wanu amachenjezedwa nawo;
powasunga pali mphotho yayikulu.
12Ndani angathe kudziwa zolakwa zake?
Mundikhululukire zolakwa zanga zobisika.
13Muteteze mtumiki wanunso ku machimo ochita akudziwa;
iwo asandilamulire.
Kotero ndidzakhala wosalakwa,
wopanda mlandu wa tchimo lalikulu.
14Mawu a mʼkamwa mwanga ndi zolingalira za mu mtima mwanga
zikhale zokondweretsa pamaso panu,
Inu Yehova, Thanthwe langa ndi Mpulumutsi wanga.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.