1Aisraeli anagonjetsa dziko lonse la kummawa kwa Yorodani, kuyambira ku chigwa cha Arinoni mpaka ku phiri la Herimoni pamodzi ndi dera lonse la kummawa kwa Araba. Iwo anatenga dzikoli kukhala lawo, ndipo mafumu a dzikoli anali awa:
2Sihoni mfumu ya Aamori,
amene ankakhala mu Hesiboni. Iye analamulira kuyambira ku Aroeri mzinda umene uli mʼmphepete mwa mtsinje wa Arinoni, mpaka ku mtsinje wa Yaboki, umene uli mʼmalire mwa Aamori, kuphatikizanso theka la dziko la Giliyadi.
3Iye ankalamuliranso dera la chigwa cha Yorodani kuyambira ku Nyanja ya Kinereti, kummawa ndi kumatsika mpaka ku Beti-Yesimoti, mzinda umene unali kummawa kwa Nyanja ya Mchere ndi kutsikabe kummwera mpaka pa tsinde pa phiri la Pisiga.
4Ogi mfumu ya mzinda wa Basani,
amene anali mmodzi mwa otsala mwa Arefaimu. Iye ankakhala ku Asiteroti ndi Ederi.
5Dera la ufumu wake linafika ku phiri la Herimoni, ku Saleka ndi dziko lonse la Basani mpaka ku malire ndi anthu a ku Gesuri Makati. Ufumu wake unaphatikizanso theka la Giliyadi mpaka ku malire a mfumu Sihoni ya ku Hesiboni.
6Mose mtumiki wa Yehova ndi Aisraeli anawagonjetsa ndipo anapereka dziko lawo kwa anthu a fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi theka la fuko la Manase kuti chikhale cholowa chawo.
7Yoswa ndi Aisraeli onse anagonjetsa mafumu onse okhala kumadzulo kwa mtsinje wa Yorodani kuyambira ku Baala-Gadi, ku chigwa cha Lebanoni mpaka ku phiri la Halaki, kumapita cha ku Seiri. Yoswa anagawira dzikolo mafuko a Israeli kuti likhale cholowa chawo.
8Dziko limeneli linali dera la ku mapiri, chigwa cha kumadzulo, chigwa cha Yorodani, ku matsitso a kummawa, ndi dziko la chipululu la kummwera. Amene ankakhala mʼdzikoli anali Ahiti, Aamori, Akanaani, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi. Mafumu ake anali awa:
9mfumu ya Yeriko
imodzi
mfumu ya Ai (kufupi ndi Beteli
imodzi
10mfumu ya Yerusalemu
imodzi
mfumu ya Hebroni
imodzi
11mfumu ya Yarimuti
imodzi
mfumu ya Lakisi
imodzi
12mfumu ya Egiloni
imodzi
mfumu ya Gezeri
imodzi
13mfumu ya Debri
imodzi
mfumu ya Gederi
imodzi
14mfumu ya Horima
imodzi
mfumu ya Aradi
imodzi
15mfumu ya Libina
imodzi
mfumu ya Adulamu
imodzi
16mfumu ya Makeda
imodzi
mfumu ya Beteli
imodzi
17mfumu ya Tapuwa
imodzi
mfumu ya Heferi
imodzi
18mfumu ya Afeki
imodzi
mfumu ya Lasaroni
imodzi
19mfumu ya Madoni
imodzi
mfumu ya Hazori
imodzi
20mfumu ya Simuroni Meroni
imodzi
mfumu ya Akisafu
imodzi
21mfumu ya Taanaki
imodzi
mfumu ya Megido
imodzi
22mfumu ya Kadesi
imodzi
mfumu ya Yokineamu ku Karimeli
imodzi
23mfumu ya Dori ku Nafoti Dori
imodzi
mfumu ya Goyini ku Giligala
imodzi
24mfumu ya Tiriza
imodzi
mafumu onse pamodzi analipo 31.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.