Masalimo 133 - The Word of God in Contemporary Chichewa

Salimo 133Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

1Onani, nʼkokoma ndi kokondweretsa ndithu

pamene abale akhala pamodzi mwachiyanjano!

2Zili ngati mafuta amtengowapatali othiridwa pa mutu,

otsikira ku ndevu,

ku ndevu za Aaroni,

oyenderera mpaka mʼkhosi mwa mkanjo wake.

3Zili ngati mame a ku Heremoni

otsikira pa Phiri la Ziyoni.

Pakuti pamenepo Yehova amaperekapo dalitso,

ndiwo moyo wamuyaya.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help