1Khoma linamangidwa ndipo zitseko zinayikidwa. Pambuyo pake alonda a Nyumba ya Mulungu, oyimba nyimbo ndiponso Alevi anasankhidwa.
2Kenaka ine ndinasankha mʼbale wanga Hanani pamodzi ndi Hananiya woyangʼanira nsanja yankhondo kukhala olamulira Yerusalemu chifukwa iyeyu anali munthu odalirika ndi woopa Mulungu kuposa anthu ena.
3Ine ndinawawuza kuti, “Musalole kuti zipata za Yerusalemu zitsekulidwe mpaka dzuwa litatentha, ndipo alonda asanaweruke aonetsetse kuti atseka zitseko ndi kuzipiringidza. Musankhe alonda pakati pa anthu okhala mu Yerusalemu, ena akhale pa malo pawo ndi ena akhale moyangʼanana ndi nyumba zawo.”
Mndandanda wa Anthu Oyamba Kubwera Kuchokera ku Ukapolo4Tsono mzinda wa Yerusalemu unali wotambasuka ndiponso waukulu koma munali anthu ochepa ndipo nyumba zinali zisanamangidwe.
5Ndipo Mulungu wanga anayika mu mtima mwanga maganizo oti ndisonkhanitse anthu olemekezeka, akuluakulu ndi anthu onse kuti alembetse mayina mwa mabanja awo. Ndinapeza buku limene munalembedwa mayina a mabanja a iwo amene anayamba kubwera kuchokera ku ukapolo. Izi ndi zimene ndinazipeza zitalembedwa mʼmenemo:
6Awa ndi anthu a mʼchigawo cha Yuda amene anabwerera kuchokera ku ukapolo amene Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anawatenga ukapolo. Iwo anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense ku mzinda wa makolo ake.
7Anabwera pamodzi ndi atsogoleri awa: Zerubabeli, Yesuwa, Nehemiya, Azariya, Raamiya, Nahamani, Mordekai, Bilisani, Misipereti, Bigivai, Nehumu ndi Baana.
Tsono chiwerengero cha anthu a ku Israeli chinali chotere:
8Zidzukulu za Parosi
2,172
9Zidzukulu za Sefatiya
372
10Zidzukulu za Ara
652
11Zidzukulu za Pahati-Mowabu (kudzera mu mʼbado wa Yesuwa ndi Yowabu)
2,818
12Zidzukulu za Elamu
1,254
13Zidzukulu za Zatu
845
14Zidzukulu za Zakai
760
15Zidzukulu za Binuyi
648
16Zidzukulu za Bebai
628
17Zidzukulu za Azigadi
2,322
18Zidzukulu za Adonikamu
667
19Zidzukulu za Abigivai
2,067
20Zidzukulu za Adini
655
21Zidzukulu za Ateri (kudzera mwa Hezekiya)
98
22Zidzukulu za Hasumu
328
23Zidzukulu za Bezayi
324
24Zidzukulu za Harifu
112
25Zidzukulu za Gibiyoni
95.
26Anthu a ku Betelehemu ndi Netofa
188
27Anthu a ku Anatoti
128
28Anthu a ku Beti-Azimaveti
42
29Anthu a ku Kiriati Yeyarimu Kefira ndi Beeroti
743
30Anthu a ku Rama ndi Geba
621
31Anthu a ku Mikimasi
122
32Anthu a ku Beteli ndi Ai
123
33Anthu a ku Nebo winayo
52
34Ana a Elamu wina
1,254
35Zidzukulu za Harimu
320
36Zidzukulu za Yeriko
345
37Zidzukulu za Lodi, Hadidi ndi Ono
721
38Zidzukulu za Senaya
3,930.
39Ansembe anali awa:
A banja la Yedaya (ndiye kuti zidzukulu za Yesuwa)
973
40Zidzukulu za Imeri
1,052
41Zidzukulu za Pasi-Huri
1,247
42Zidzukulu za Harimu
1,017.
43Alevi anali awa:
A banja la Yesuwa ndi Kadimieli, ndiye kuti zidzukulu za Hodaviya
74.
44Anthu oyimba:
Zidzukulu za Asafu
148.
45Alonda a ku Nyumba ya Mulungu anali awa:
Zidzukulu za
Salumu, Ateri, Talimoni, Hatita ndi Sobai
138.
46Anthu ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu anali awa:
Zidzukulu za
Ziha, zidzukulu za Hasufa, zidzukulu za Tabaoti,
47Zidzukulu Kerosi, zidzukulu za Siya, zidzukulu za Padoni
48Zidzukulu za Lebana za Hagaba, ndi za Salimayi,
49Zidzukulu za Hanani, zidzukulu za Gideli, zidzukulu za Gahari,
50Zidzukulu za Reyaya, zidzukulu za Rezini, zidzukulu za Nehoda,
51Zidzukulu za Gazamu, zidzukulu za Uza, zidzukulu za Paseya,
52Zidzukulu za Besai, zidzukulu za Meunimu, zidzukulu za Nefusimu,
53Zidzukulu za Bakibuku, zidzukulu za Hakufa, zidzukulu za Harihuri,
54Zidzukulu za Baziliti, zidzukulu za Mehida, zidzukulu za Harisa,
55Zidzukulu za Barikosi, zidzukulu za Sisera, zidzukulu za Tema
56Zidzukulu za Neziya, ndi zidzukulu za Hatifa.
57Zidzukulu za antchito a Solomoni:
Zidzukulu za
Sotai, zidzukulu za Sofereti, zidzukulu za Perida
58zidzukulu za Yaala, zidzukulu za Darikoni, zidzukulu za Gideli,
59zidzukulu za Sefatiya, zidzukulu za Hatilu
zidzukulu za Pokereti-Hazebaimu ndi zidzukulu Amoni.
60Anthu onse ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi zidzukulu za antchito a Solomoni analipo
392.
61Ali munsiwa anachokera ku Teli-Mela, Teri-Harisa, Kerubi, Adoni, ndi Imeri, koma sanathe kunena mwa tchutchutchu kuti makolo awo kapena mafuko awo analidi Aisraeli kapena ayi.
62Zidzukulu za
Delaya, zidzukulu za Tobiya ndi zidzukulu za Nekoda
642.
63Ndiponso ena pakati pa ansembe anali awa:
zidzukulu za
Hobiya, zidzukulu za Hakozi ndi zidzukulu za Barizilai (munthu amene anakwatira mwana wamkazi wa Barizilai wa ku Giliyadi ndipo amatchedwa dzina limenelo).
64Iwowa anafufuzafufuza mayina awo mʼbuku la mibado ya mabanja awo ndipo sanapeze mayina awo kotero anachotsedwa pa unsembe nawerengedwa ngati odetsedwa pa chipembedzo.
65Choncho bwanamkubwa anawawuza anthuwo kuti asamadye nawo chakudya china chilichonse choperekedwa kwa Mulungu mpaka patapezeka wansembe wodziwa kugwiritsa bwino ntchito ya Urimu ndi Tumimu.
66Chiwerengero chonse cha anthuwa chinali 42,360.
67Kuwonjezera pamenepa panali antchito awo aamuna ndi aakazi 7,337 ndiponso anthu aamuna ndi aakazi oyimba nyimbo okwanira 245.
68Panali akavalo 736, abulu angʼonoangʼono 245.
69Ngamira zawo zinalipo 435 ndipo abulu analipo 6,720.
70Atsogoleri ena a mabanja anapereka mphatso zothandizira ntchito. Bwanamkubwa anapereka ku thumba losungira chuma, ndalama zagolide za makilogalamu asanu ndi atatu, mabeseni makumi asanu ndi zovala za ansembe 530.
71Atsogoleri ena amabanja anapereka ku thumba losungira chuma ndalama zagolide zokwana makilogalamu 168, ndiponso ndalama za siliva zokwana makilogalamu 1,250.
72Anthu ena onse otsala anapereka ndalama zagolide zokwana makilogalamu 168, ndalama za siliva zokwana makilogalamu 140, ndiponso zovala za ansembe 67.
73Choncho ansembe, Alevi, alonda a Nyumba ya Mulungu, anthu oyimba nyimbo, ena mwa anthu wamba, ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi Aisraeli ena onse ankakhala mʼmizinda yawo.
Ezara Awerenga MalamuloPofika mwezi wachisanu ndi chiwiri Aisraeli onse anali atakhazikika mʼmizinda yawo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.