Masalimo 140 - The Word of God in Contemporary Chichewa

Salimo 140Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

1Landitseni Yehova kwa anthu oyipa;

tetezeni kwa anthu ankhanza,

2amene mu mtima mwawo amakonza zinthu zoyipa

ndi kuyambitsa nkhondo tsiku lililonse.

3Iwo amanola malilime awo kukhala akuthwa ngati a njoka;

pa milomo yawo pali ululu wa mamba.

Sela

4Tetezeni Inu Yehova, kwa anthu oyipa;

tchinjirizeni kwa anthu ankhanza

amene amakonza zokola mapazi anga.

5Anthu odzikuza anditchera msampha mobisika;

iwo atchera zingwe za maukonde awo

ndipo anditchera misampha pa njira yanga.

Sela

6Inu Yehova, ine ndikuti, “Ndinu Mulungu wanga.”

Imvani kupempha kwanga Yehova.

7Inu Ambuye Wamphamvuzonse, Mpulumutsi wanga wamphamvu,

mumateteza mutu wanga tsiku lankhondo.

8Musawapatse anthu oyipa zokhumba zawo, Inu Yehova;

musalole kuti zokonza zawo zitheke,

mwina iwo adzayamba kunyada.

Sela

9Mitu ya amene andizungulira

iphimbidwe ndi masautso amene milomo yawo yayambitsa.

10Makala amoto agwere pa iwo;

aponyedwe pa moto,

mʼmaenje amatope, asatulukemonso.

11Musalole kuti anthu achipongwe akhazikike mʼdziko;

choyipa chilondole anthu ankhanza.

12Ndikudziwa kuti Yehova amapereka chiweruzo cholungama kwa anthu osauka,

ndipo amateteza zolinga za anthu osowa.

13Zoonadi anthu olungama adzatamanda dzina lanu,

ndipo anthu owongoka mtima adzakhala pamaso panu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help