Yesaya 50 - The Word of God in Contemporary Chichewa

Tchimo la Israeli, Kumvera kwa Mtumiki

1Yehova akuti,

“Kalata imene ndinasudzulira amayi

anu ili kuti?

Kapena mwa anthu amene ndili nawo ngongole,

ndinakugulitsani kwa ati?

Inu munagulitsidwa ku ukapolo chifukwa cha machimo anu;

amayi anu anachotsedwa chifukwa cha kulakwa kwanu.

2Nʼchifukwa chiyani pamene ndinabwera kudzakupulumutsani panalibe munthu?

Pamene ndinayitana, nʼchifukwa chiyani panalibe wondiyankha?

Kodi dzanja langa ndi lalifupi kuti nʼkulephera kukuwombolani?

Kodi ndilibe mphamvu zokupulumutsirani?

Ndi kudzudzula kokha ndinawumitsa nyanja yayikulu,

mitsinje ndinayisandutsa chipululu;

nsomba za mʼmenemo zinawola chifukwa chosowa madzi;

ndipo zinafa ndi ludzu.

3Ndinaphimba thambo ndi mdima

ndipo chiguduli chinakhala chofunda chake.”

4Ambuye Yehova anandiphunzitsa mawu oyenera kuyankhula

kudziwa mawu olimbitsa mtima anthu ofowoka.

Mmawa mulimonse amandidzutsa,

amathwetsa khutu langa kuti ndimve monga amachitira munthu amene akuphunzira.

5Ambuye Yehova wanditsekula makutu anga,

ndipo sindinakhale munthu wowukira

ndipo sindinabwerere mʼmbuyo.

6Ndinapereka msana wanga kwa ondimenya

masaya anga ndinawapereka kwa anthu ondizula ndevu;

sindinawabisire nkhope yanga

anthu ondinyoza ndi ondilavulira.

7Popeza Ambuye Yehova amandithandiza,

sindidzachita manyazi.

Tsono ndalimba mtima ngati msangalabwi,

chifukwa ndikudziwa kuti sindidzachita manyazi.

8Wondikhalira kumbuyo ali pafupi,

ndaninso amene adzandiyimba mlandu?

Abwere kuti tionane maso ndi maso!

Mdani wanga ndi ndani?

Abweretu kuti tilimbane!

9Ambuye Yehova ndiye amene amandithandiza.

Ndaninso amene adzanditsutsa?

Onse adzatha ngati chovala

chodyedwa ndi njenjete.

10Ndani mwa inu amaopa Yehova

ndi kumvera mawu a mtumiki wake?

Aliyense woyenda mu mdima,

popanda chomuwunikira,

iye akhulupirire dzina la Yehova

ndi kudalira Mulungu wake.

11Koma tsopano inu nonse amene mumasonkha moto

ndi kuyatsa sakali za moto kufuna kuwononga anzanu,

lowani mʼmoto wanu womwewo.

Pitani mu sakali za moto zimene mwayatsa.

Ndipo ine Yehova

ndiye amene ndidzakugwetsereni mazunzowo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help