Masalimo 29 - The Word of God in Contemporary Chichewa

Salimo 29Salimo la Davide.

1Perekani kwa Yehova, inu anthu amphamvu,

perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu.

2Perekani kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake,

pembedzani Yehova mwa kukongola kwa chiyero chake.

3Liwu la Yehova lili pamwamba pa madzi;

Mulungu waulemerero abangula,

Yehova abangula pamwamba pa madzi amphamvu.

4Liwu la Yehova ndi lamphamvu;

liwu la Yehova ndi laulemerero.

5Liwu la Yehova limathyola mikungudza;

Yehova amathyolathyola mikungudza ya ku Lebanoni.

6Iye amachititsa Lebanoni kulumphalumpha ngati mwana wangʼombe,

Siriyoni ngati mwana wa njati:

7Liwu la Yehova limakantha

ngati kungʼanima kwa mphenzi.

8Liwu la Yehova limagwedeza chipululu;

Yehova amagwedeza chipululu cha Kadesi.

9Liwu la Yehova limapindapinda mibawa

ndi kuyeretsa nkhalango.

Ndipo mʼNyumba mwake onse amafuwula kuti, “Ulemerero!”

10Yehova amakhala pamwamba pa madzi osefukira,

Yehova ndiye mfumu kwamuyaya.

11Yehova amapereka mphamvu kwa anthu ake;

Yehova amadalitsa anthu ake ndi mtendere.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help