Masalimo 53 - The Word of God in Contemporary Chichewa

Salimo 53Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a Mahalati. Ndakatulo ya Davide.

1Chitsiru chimati mu mtima mwake,

“Kulibe Mulungu.”

Iwo ndi oyipa ndipo njira zawo ndi zonyansa;

palibe ndi mmodzi yemwe amene amachita chabwino.

2Mulungu kumwamba amayangʼana pansi pano

pa ana a anthu

kuti aone ngati alipo wina wanzeru,

wofunafuna Mulungu.

3Aliyense wabwerera,

iwo onse pamodzi akhala oyipa;

palibe ndi mmodzi yemwe amene amachita chabwino,

ngakhale mmodzi.

4Kodi anthu ochita zoyipawa adzaphunziradi;

anthu amene amadya anthu anga monga mmene anthu amadyera buledi,

ndipo sapemphera kwa Mulungu?

5Iwo anali pamenepo atathedwa nzeru ndi mantha aakulu

pamene panalibe kanthu kochititsa mantha.

Mulungu anamwazamwaza mafupa a anthu amene anakuthirani nkhondo;

inuyo munawachititsa manyazi, pakuti Mulungu anawanyoza.

6Ndithu, chipulumutso cha Israeli nʼchochokera ku Ziyoni!

Pamene Mulungu adzabwezeretsanso ulemerero wa anthu ake,

lolani Yakobo akondwere ndi Israeli asangalale!

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help