Masalimo 91 - The Word of God in Contemporary Chichewa

Salimo 91

1Iye amene amakhala mu mthunzi wa Wammwambamwamba

adzapuma mu mthunzi wa Wamphamvuzonse.

2Ndidzanena za Yehova, “Iye ndiye pothawira panga ndi linga langa,

Mulungu wanga amene ndimadalira.”

3Ndithu, Iye adzakupulumutsa ku msampha wa mlenje

ndi ku mliri woopsa;

4Adzakuphimba ndi nthenga zake,

ndipo udzapeza malo othawira mʼmapikomo;

kukhulupirika kwake kudzakhala chishango chako ndi lihawo.

5Sudzachita mantha ndi zoopsa za usiku,

kapena muvi wowuluka masana,

6kapena mliri umene umayenda mu mdima,

kapena zowononga za pa nthawi ya masana.

7Anthu 1,000 atha kufa pambali pako,

anthu 10,000 kudzanja lako lamanja,

koma zoopsazo sizidzafika pafupi ndi iwe.

8Udzapenya ndi maso ako

ndipo udzaona mmene anthu oyipa amalangidwira.

9Pakuti wasankha Wammwambamwamba kukhala malo ako okhalamo;

wavomera Yehova kukhala kothawira kwako.

10Choncho palibe choyipa chimene chidzakugwera,

zoopsa sizidzafika pafupi ndi tenti yako.

11Pakuti adzalamulira angelo ake za iwe,

kuti akutchinjirize mosamala pa njira zako zonse;

12ndipo adzakunyamula ndi manja awo,

kuti phazi lako lisagunde pa mwala.

13Udzapondaponda mkango ndi njoka,

udzapondereza mkango wamphamvu ndiponso chinjoka.

14“Chifukwa iye amandikonda,” akutero Yehova, “Ndidzamulanditsa;

ndidzamuteteza pakuti wavomereza dzina langa.

15Adzandiyitana, ndipo ndidzamuyankha;

ndidzakhala naye pa mavuto,

ndidzamupulumutsa ndi kumulemekeza.

16Ndidzamupatsa moyo wautali

ndi kumupulumutsa.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help