Yesaya 20 - The Word of God in Contemporary Chichewa

Za Chilango cha Igupto ndi Kusi

1Mʼchaka chimene mkulu wankhondo wotumidwa ndi mfumu ya ku Asiriya, anabwera ku Asidodi ndi kuwuthira nkhondo ndi kuwulanda,

2nthawi imeneyo Yehova anawuza Yesaya mwana wa Amozi kuti, “Pita kavule chiguduli ndi nsapato zako.” Ndipo iye anaterodi, ankangoyenda wamaliseche ndiponso wopanda nsapato.

3Kenaka Yehova anati, “Monga momwe mtumiki wanga Yesaya wakhala akuyendera wamaliseche ndiponso wopanda nsapato kwa zaka zitatu ngati chizindikiro ndi chenjezo kwa dziko la Igupto ndi Kusi,

4momwemonso mfumu ya ku Asiriya idzatenga ukapolo anthu a ku Igupto ndi a ku Kusi, anyamata ndi okalamba. Iwo adzakhala amaliseche ndi opanda nsapato, matako ali pa mtunda. Zimenezi zidzachititsa manyazi Igupto.

5Amene ankadalira Kusi, ndiponso amene ankadzitukumula chifukwa cha Igupto adzakhumudwa ndi kuchita manyazi.

6Tsiku limenelo anthu amene amakhala mʼmbali mwa nyanja adzati, ‘Taonani zomwe zawachitikira amene ife tinkawadalira, amene ife tinkathawirako kuti atithandize ndi kutipulumutsa kwa mfumu ya ku Asiriya! Nanga ife tidzapulumuka bwanji?’ ”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help