1Odala ndi onse amene amaopa Yehova,
amene amayenda mʼnjira zake.
2Udzadya chipatso cha ntchito yako;
madalitso ndi chuma zidzakhala zako.
3Mkazi wako adzakhala ngati mpesa wobereka
mʼkati mwa nyumba yako;
ana ako adzakhala ngati mphukira za mitengo ya olivi
kuzungulira tebulo lako.
4Ameneyu ndiye munthu wodalitsidwa
amene amaopa Yehova.
5Yehova akudalitse kuchokera mʼZiyoni
masiku onse a moyo wako;
uwone zokoma za Yerusalemu,
6ndipo ukhale ndi moyo kuti udzaone zidzukulu zako.
Mtendere ukhale ndi Israeli.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.