Masalimo 70 - The Word of God in Contemporary Chichewa

Salimo 70Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Pempho.

1Fulumirani Mulungu kundipulumutsa;

Yehova bwerani msanga kudzandithandiza.

2Iwo amene akufunafuna moyo wanga

achititsidwe manyazi ndi kusokonezedwa;

onse amene akukhumba chiwonongeko changa

abwezedwe mopanda ulemu.

3Onse amene akunena kwa ine kuti, “Aha, aha,”

abwerere chifukwa cha manyazi awo.

4Koma onse amene akufunafuna Inu

akondwere ndi kusangalala mwa Inu;

iwo amene amakonda chipulumutso chanu

nthawi zonse anene kuti, “Mulungu akuzike!”

5Koma ine ndine wosauka ndi wosowa;

bwerani msanga kwa ine Inu Mulungu.

Inu ndinu thandizo langa ndi momboli wanga;

Inu Yehova musachedwe.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help