Yeremiya 47 - The Word of God in Contemporary Chichewa

Uthenga Wonena za Afilisti

1Uthenga umene Yehova anamupatsa mneneri Yeremiya wonena za Afilisti, Farao asanathire nkhondo Gaza ndi uwu:

2Yehova akuti,

“Taonani mmene madzi akubwerera kuchokera kumpoto;

adzasanduka mtsinje wosefukira ndi a mkokomo.

Adzasefukira mʼdziko monse ndi kumiza chilichonse mʼmenemo,

mizinda ndi onse okhala mʼmenemo.

Anthu adzafuwula;

anthu onse okhala mʼdzikomo adzalira

3akadzamva mgugu wa ngʼombe zazimuna zothamanga,

phokoso la magaleta ake

ndi kulira kwa mikombero yake.

Makolo sadzatembenuka kuti athandize ana awo;

manja awo adzangoti khoba.

4Pakuti tsiku lafika

lowononga Afilisti onse

ndi kupha onse otsala,

onse amene akanatha kuthandiza Turo ndi Sidoni.

Yehova ali pafupi kuwononga Afilisti,

otsala ochokera ku zilumba za ku Kafitori.

5Anthu a ku Gaza ameta mipala;

anthu a ku Asikeloni akhala chete.

Inu otsala a ku chigwa,

mudzakhala mukudzichekacheka mpaka liti?

6“Mukulira kuti, ‘Aa, lupanga la Yehova,

kodi udzapumula liti?

Bwerera mʼmalo ako;

ukhale momwemo ndipo ukhale chete.’

7Koma lupangalo lidzapumula bwanji

pamene Yehova walilamulira

kuti lithire nkhondo

Asikeloni ndi anthu a mʼmbali mwa nyanja?”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help