Yesaya 61 - The Word of God in Contemporary Chichewa

Uthenga Wabwino wa Yehova

1Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine,

chifukwa Yehova wandidzoza

kuti ndilalikire uthenga wabwino kwa anthu osauka.

Wandituma kuti ndikatonthoze anthu osweka mtima,

ndikalengeze kwa akapolo kuti alandire ufulu

ndiponso kuti ndikamasule a mʼndende.

2Wandituma kuti ndikalengeze nthawi imene Yehova adzapulumutsa anthu ake;

za tsiku limene Yehova adzalanga adani a anthu ake.

Wandituma kuti ndikatonthoze olira.

3Wandituma kuti ndiwakonzere olira a ku Ziyoni,

nkhata ya maluwa yokongola

mʼmalo mwa phulusa,

ndiwapatse mafuta achikondwerero

mʼmalo mwa kulira.

Ndiwapatse chovala cha matamando

mʼmalo mwa mtima wopsinjika.

Ndipo iwo adzatchedwa mitengo ya thundu yamphamvu yachilungamo,

yoyidzala Yehova

kuti Iye mwini apezemo ulemerero wake.

4Adzamanganso mabwinja akale a mzinda

ndipo malo amene anawonongeka kalekale aja adzakonzanso.

Adzakonzanso mizinda imene inapasuka,

imene yakhala yowonongeka kwa nthawi yayitali kwambiri.

5Anthu achilendo adzakutumikirani; adzazidyetsa ziweto zanu;

iwo adzagwira ntchito mʼminda yanu ya mpesa.

6Ndipo inu mudzatchedwa ansembe a Yehova,

adzakutchulani kuti ndinu atumiki a Mulungu wathu.

Mudzadyerera chuma cha mitundu ya anthu,

ndipo mudzanyadira ulemu umene mwalandira.

7Chifukwa manyazi awo anali owirikiza;

ndi kuti munalandira

chitonzo ndi kutukwana,

adzakondwera ndi cholowa chawo,

tsono adzalandira cholowa chawo cha chigawo cha dziko mowirikiza,

ndipo chimwemwe chamuyaya chidzakhala chawo.

8“Pakuti Ine Yehova, ndimakonda chilungamo;

ndimadana ndi zakuba ndi zoyipa.

Anthu anga ndidzawapatsa mphotho mokhulupirika

ndikupangana nawo pangano losatha.

9Ana awo adzakhala odziwika pakati pa mitundu ya anthu

ndipo adzukulu awo adzakhala otchuka pakati pa anthu a mitundu ina.

Aliyense wowaona adzazindikira

kuti ndi anthu amene Yehova wawadalitsa.”

10Ine ndikusangalala kwambiri chifukwa cha Yehova;

moyo wanga ukukondwera chifukwa cha Mulungu wanga.

Pakuti Iye wandiveka zovala zachipulumutso,

ndipo wandiveka mkanjo wachilungamo.

Zili ngati mkwati wovala nkhata ya maluwa mʼkhosi mwake,

ndiponso ngati mkwatibwi wovala mikanda yamtengowapatali.

11Monga momwe nthaka imameretsa mbewu

ndiponso monga munda umakulitsa mbewu zimene anadzala,

momwemonso Ambuye Yehova adzaonetsa chilungamo ndi matamando

pamaso pa mitundu yonse ya anthu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help