Masalimo 75 - The Word of God in Contemporary Chichewa

Salimo 75Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe, potsata mayimbidwe a “Musawononge.” Salimo la Asafu. Nyimbo.

1Tikuthokoza Inu Mulungu,

tikuthokoza, pakuti dzina lanu lili pafupi nafe,

anthutu amafotokoza za ntchito zanu zodabwitsa.

2Mumati, “Ine ndimayika nthawi yoyenera,

ndine amene ndimaweruza mwachilungamo.

3Pamene dziko lapansi ndi anthu ake onse anjenjemera,

ndine amene ndimagwiriziza mizati yake molimba.

Sela

4Kwa odzitama ndikuti, ‘Musadzitamenso,’

ndipo kwa oyipa, ‘Musatukulenso nyanga zanu.

5Musatukule nyanga zanu motsutsana ndi kumwamba;

musayankhule ndi khosi losololoka.’ ”

6Kugamula milandu sikuchokera kummawa kapena kumadzulo

kapena ku chipululu.

7Koma ndi Mulungu amene amaweruza:

Iyeyo amatsitsa wina, nakwezanso wina.

8Mʼdzanja la Yehova muli chikho

chodzaza ndi vinyo wochita thovu, wosakanizidwa ndi zokometsera;

Iye amamutsanulira pansi ndipo onse oyipa a dziko lapansi

amamwa ndi senga zake zonse.

9Kunena za ine, ndidzalengeza izi kwamuyaya;

ndidzayimba matamando kwa Mulungu wa Yakobo.

10Ndidzadula nyanga za onse oyipa

koma nyanga za olungama zidzakwezedwa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help