Masalimo 120 - The Word of God in Contemporary Chichewa

Salimo 120Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

1Ndimafuwulira kwa Yehova mʼmasautso anga,

ndipo Iye amandiyankha.

2Pulumutseni Yehova ku milomo yabodza,

ndi kwa anthu achinyengo.

3Kodi adzakuchitani chiyani,

ndipo adzawonjezerapo zotani, inu anthu achinyengo?

4Adzakulangani ndi mivi yakuthwa ya munthu wankhondo,

ndi makala oyaka a mtengo wa tsanya.

5Tsoka ine kuti ndimakhala ku Mesaki,

kuti ndimakhala pakati pa matenti a ku Kedara!

6Kwa nthawi yayitali ndakhala pakati

pa iwo amene amadana ndi mtendere.

7Ine ndine munthu wamtendere;

koma ndikamayankhula, iwo amafuna nkhondo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help