1Yehova atikomere mtima ndi kutidalitsa,
achititse kuti nkhope yake itiwalire.
2Kuti njira zanu zidziwike pa dziko lapansi,
chipulumutso chanu pakati pa mitundu yonse.
3Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu;
mitundu yonse ya anthu ikutamandeni.
4Mitundu yonse ya anthu isangalale ndi kuyimba mwachimwemwe,
pakuti inu mumaweruza mitundu ya anthu mwachilungamo
ndi kutsogolera mitundu ya anthu a dziko lapansi.
5Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu;
mitundu yonse ya anthu ikutamandeni.
6Nthaka yabereka zokolola zake;
tidalitseni Mulungu wathu.
7Mulungu atidalitse
kuti pamenepo malekezero onse a dziko lapansi apembedze Iyeyo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.