Masalimo 148 - The Word of God in Contemporary Chichewa

Salimo 148

1Tamandani Yehova.

Tamandani Yehova, inu a kumwamba,

mutamandeni Iye, inu a mlengalenga.

2Mutamandeni, inu angelo ake onse,

mutamandeni, mutamandeni, inu zolengedwa za mmwamba.

3Mutamandeni, inu dzuwa ndi mwezi,

mutamandeni, inu nonse nyenyezi zowala.

4Mutamandeni, inu thambo la kumwambamwamba

ndi inu madzi a pamwamba pa thambo.

5Zonse zitamande dzina la Yehova

pakuti Iye analamula ndipo zinalengedwa.

6Iye anaziyika pa malo ake ku nthawi za nthawi;

analamula ndipo sizidzatha.

7Tamandani Yehova pa dziko lapansi,

inu zolengedwa zikuluzikulu za mʼnyanja, ndi nyanja zonse zakuya,

8inu zingʼaningʼani ndi matalala, chipale ndi mitambo,

mphepo yamkuntho imene imakwaniritsa mawu ake,

9inu mapiri ndi zitunda zonse,

inu mitengo ya zipatso ndi mikungudza yonse,

10inu nyama zakuthengo ndi ngʼombe zonse,

inu zolengedwa zingʼonozingʼono ndi mbalame zowuluka.

11Inu mafumu a dziko lapansi ndi anthu a mitundu yonse,

inu akalonga ndi olamulira a dziko lapansi.

12Inu anyamata ndi anamwali,

inu nkhalamba ndi ana omwe.

13Onsewo atamande dzina la Yehova

pakuti dzina lake lokha ndi lolemekezeka;

ulemerero wake ndi woopsa pa dziko lapansi pano ndi kumwamba komwe.

14Iye wakwezera nyanga anthu ake,

matamando a anthu ake onse oyera mtima,

Aisraeli, anthu a pamtima pake.

Tamandani Yehova.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help