Hoseya 12 - The Word of God in Contemporary Chichewa

1Efereimu amadya mpweya;

tsiku lonse amasaka mphepo ya kummawa

ndipo amachulukitsa mabodza ndi chiwawa.

Amachita mgwirizano ndi Asiriya

ndipo amatumiza mphatso za mafuta a olivi ku Igupto.

2Yehova akuyimba mlandu Yuda;

Iye adzalanga Yakobo molingana ndi makhalidwe ake,

adzamulanga molingana ndi ntchito zake.

3Akali mʼmimba mwa amayi ake, Yakobo anagwira chidendene cha mʼbale wake;

iye atakula analimbana ndi Mulungu.

4Yakobo analimbana ndi mngelo ndipo anapambana;

analira napempha kuti amukomere mtima.

Mulungu anakumana naye ku Beteli

ndipo anayankhula naye kumeneko,

5Yehova Mulungu Wamphamvuzonse,

Yehova ndiye dzina lake lotchuka!

6Koma inu muyenera kubwerera kwa Mulungu wanu;

pitirizani chikondi ndi chiweruzo cholungama,

ndipo muzidikira Mulungu wanu nthawi zonse.

7Munthu wamalonda amagwiritsa ntchito masikelo achinyengo;

iyeyo amakonda kubera anthu.

8Efereimu amadzitama ponena kuti,

“Ndine wolemera kwambiri; ndili ndi chuma chambiri.

Palibe amene angandiloze chala

chifukwa cha kulemera kwanga.”

9“Ine ndine Yehova Mulungu wako

amene ndinakutulutsa mu Igupto.

Ndidzakukhazikaninso mʼmatenti,

monga munkachitira masiku aja pa nthawi ya zikondwerero zanu.

10Ndinayankhula ndi aneneri,

ndinawaonetsa masomphenya ambiri,

ndipo ndinawawuza mafanizo kudzera mwa iwo.”

11Kodi Giliyadi ndi woyipa?

Anthu ake ndi achabechabe!

Kodi amapereka nsembe za ngʼombe zazimuna ku Giligala?

Maguwa awo ansembe adzakhala ngati milu ya miyala

mʼmunda molimidwa.

12Yakobo anathawira ku dziko la Aramu,

Israeli anagwira ntchito kuti apeze mkazi,

ndipo anaweta nkhosa kuti akwatire mkaziyo.

13Yehova anagwiritsa ntchito mneneri kuti atulutse Israeli mu Igupto;

kudzera mwa mneneriyo Iye anawasamalira.

14Koma Efereimu wamukwiyitsa kwambiri.

Nʼchifukwa chake Yehova adzawalanga ndi imfa.

Adzawalanga chifukwa anamuchititsa manyazi kwambiri.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help