Masalimo 124 - The Word of God in Contemporary Chichewa

Salimo 124Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

1Akanapanda kukhala mbali yathu Yehova,

anene tsono Israeli,

2akanapanda kukhala mbali yathu Yehova,

potiwukira anthuwo,

3iwo atatipsera mtima,

akanatimeza amoyo;

4chigumula chikanatimiza,

mtsinje ukanatikokolola,

5madzi a mkokomo

akanatikokolola.

6Atamandike Yehova,

amene sanalole kuti tikhale chakudya cha mano awo.

7Moyo wathu wawonjoka ngati mbalame

yokodwa mu msampha wa mlenje;

msampha wathyoka,

ndipo ife tapulumuka.

8Thandizo lathu lili mʼdzina la Yehova

wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help