1Mpaka liti Yehova? Kodi mudzandiyiwala mpaka kalekale?
Mpaka liti mudzandibisira nkhope yanu?
2Ndidzalimbana ndi maganizo anga
ndi kukhala ndi chisoni mu mtima mwanga tsiku lililonse mpaka liti?
Mpaka liti adani anga adzandipambana?
3Ndiyangʼaneni ndi kundiyankha, Inu Yehova Mulungu wanga.
Walitsani maso anga kuti ndingafe;
4mdani wanga adzati, “Ndamugonjetsa,”
ndipo adani anga adzakondwera pamene ine ndagwa.
5Koma ndikudalira chikondi chanu chosasinthika;
mtima wanga umakondwera ndi chipulumutso chanu.
6Ine ndidzayimbira Yehova
pakuti wandichitira zokoma.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.