Masalimo 130 - The Word of God in Contemporary Chichewa

Salimo 130Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

1Ndikulirira kwa Inu Yehova ndili mʼdzenje lozama;

2Ambuye imvani mawu anga.

Makutu anu akhale tcheru kumva

kupempha chifundo kwanga.

3Inu Yehova, mukanamawerengera machimo,

Inu Yehova, akanayima chilili ndani wopanda mlandu?

4Koma kwa Inu kuli chikhululukiro;

nʼchifukwa chake mumaopedwa.

5Ndimayembekezera Yehova, moyo wanga umayembekezera,

ndipo ndimakhulupirira mawu ake.

6Moyo wanga umayembekezera Ambuye,

kupambana momwe alonda amayembekezera mmawa,

inde, kupambana momwe alonda amayembekezera mmawa,

7Yembekeza Yehova, iwe Israeli,

pakuti Yehova ali ndi chikondi chosasinthika

ndipo alinso ndi chipulumutso chochuluka.

8Iye mwini adzawombola Israeli

ku machimo ake onse.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help