Estere 10 - The Word of God in Contemporary Chichewa

Ukulu wa Mordekai

1Mfumu Ahasiwero anakhometsa msonkho mʼdziko lake lonse mpaka ku zilumba zonse.

2Ndipo ntchito zonse zochitika ndi mphamvu zake komanso ndi zonse zofotokoza za ukulu wa Mordekai, kukwezedwa kwake ndi mfumu, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a ku Mediya ndi Peresiya?

3Pakuti Mordekai Myuda uja anali wachiwiri wa mfumu Ahasiwero. Kwa Ayuda onse Mordekai anali munthu wamkulu ndipo ankamukonda chifukwa ankachitira zabwino mtundu wake ndi kufunira mtendere abale ake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help