Masalimo 28 - The Word of God in Contemporary Chichewa

Salimo 28Salimo la Davide.

1Kwa Inu ine ndiyitana, Yehova ndinu Thanthwe langa;

musakhale osamva kwa ine.

Pakuti mukapitirira kukhala chete,

ndidzakhala ngati iwo amene atsikira ku dzenje.

2Imvani kupempha chifundo kwanga

pomwe ndikuyitana kwa Inu kuti mundithandize,

pomwe ndikukweza manja anga

kuloza ku malo anu oyeretsetsa.

3Musandikokere kutali pamodzi ndi anthu oyipa,

pamodzi ndi iwo amene amachita zoyipa,

amene amayankhula mwachikondi ndi anzawo

koma akusunga chiwembu mʼmitima mwawo.

4Muwabwezere chifukwa cha zochita zawo

ndi ntchito zawo zoyipa;

abwezereni chifuwa cha zimene manja awo achita

ndipo mubweretse pa iwo zimene zowayenera.

5Popeza iwowo sakhudzidwa ndi ntchito za Yehova,

ndi zimene manja ake anazichita,

Iye adzawakhadzula

ndipo sadzawathandizanso.

6Matamando apite kwa Yehova,

popeza Iye wamva kupempha chifundo kwanga.

7Yehova ndiye mphamvu yanga ndi chishango changa;

mtima wanga umadalira Iye, ndipo Ine ndathandizidwa.

Mtima wanga umalumphalumpha chifukwa cha chimwemwe

ndipo ndidzayamika Iye mʼnyimbo.

8Yehova ndi mphamvu ya anthu ake,

linga la chipulumutso kwa wodzozedwa wake.

9Pulumutsani anthu anu ndipo mudalitse cholowa chanu;

mukhale mʼbusa wawo ndipo muwakweze kwamuyaya.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help