Masalimo 26 - The Word of God in Contemporary Chichewa

Salimo 26Salimo la Davide.

1Weruzeni Inu Yehova

pakuti ndakhala moyo wosalakwa.

Ndadalira Yehova

popanda kugwedezeka.

2Patseni mayeso, Inu Yehova ndipo ndiyeseni,

santhulani mtima wanga ndi maganizo anga;

3pakuti chikondi chanu chili pamaso panga nthawi zonse,

ndipo ndimayenda mʼchoonadi chanu nthawi zonse.

4Ine sindikhala pansi pamodzi ndi anthu achinyengo,

kapena kufunsa nzeru kwa achiphamaso.

5Ndimanyansidwa ndi msonkhano wa anthu ochita zoyipa

ndipo ndimakana kukhala pansi pamodzi ndi oyipa.

6Ndimasamba mʼmanja mwanga kuonetsa kusalakwa kwanga

ndi kupita kukatumikira pa guwa lanu la nsembe, Inu Yehova,

7kulengeza mofuwula za matamando anu

ndi kuwuza onse za ntchito zanu zodabwitsa.

8Ndimakonda Nyumba imene Inu Yehova mumakhalamo,

malo amene ulemerero wanu umapezekako.

9Musachotse moyo wanga pamodzi ndi ochimwa,

moyo wanga pamodzi ndi anthu akupha anzawo,

10amene mʼmanja mwawo muli ndondomeko zoyipa,

dzanja lawo lamanja ladzaza ndi ziphuphu.

11Koma ine ndimakhala moyo wosalakwa;

mu msonkhano wa anthu anu ndidzatamanda Yehova.

12Ndayima pa malo wopanda zovuta

ndipo ndidzatamanda Yehova mu msonkhano waukulu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help