Masalimo 20 - The Word of God in Contemporary Chichewa

Salimo 20Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

1Yehova akuyankhe pamene uli pa msautso;

dzina la Mulungu wa Yakobo likuteteze.

2Iye atumize thandizo kuchokera ku malo ake opatulika;

akugwirizize kuchokera ku Ziyoni.

3Iye akumbukire nsembe zako zonse

ndipo alandire nsembe zako zopsereza.

Sela

4Akupatse chokhumba cha mtima wako

ndipo akuthandize kuti zonse wakonza zichitike.

5Ife tidzafuwula ndi chimwemwe pamene iwe wapambana

ndipo tidzanyamula mbendera zathu mʼdzina la Mulungu wathu,

Yehova ayankhe zopempha zako zonse.

6Tsopano ndadziwa kuti Yehova amapulumutsa wodzozedwa wake;

Iye amamuyankha kuchokera kumwamba ku malo ake opatulika

ndi mphamvu yopulumutsa ya dzanja lake lamanja.

7Ena amadalira magaleta ndipo ena akavalo

koma ife tidzadalira dzina la Yehova Mulungu wathu.

8Iwo amagonjetsedwa ndi kugwa,

koma ife timadzuka ndi kuyima chilili.

9Inu Yehova, pulumutsani mfumu!

Tiyankheni pamene tikuyitanani!

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help