Yeremiya 17 - The Word of God in Contemporary Chichewa

1“Tchimo la Yuda lazokotedwa ndi cholembera cha chitsulo,

lalembedwa ndi msonga ya mwala wadayimondi.

Uchimowo walembedwa pa mitima yawo

ndiponso pa nyanga za maguwa awo.

2Ngakhale ana awo amakumbukira

maguwa awo ndi zoyimiritsa ngati zifanizo za mulungu wawo Asera,

pa tsinde la mitengo ya masamba ambiri,

pa mapiri aatali mʼdzikomo.

3Chuma chanu ndiponso katundu wanu yense

ndidzazipereka kwa ofunkha

kuti zikhale dipo lawo

chifukwa cha machimo

ochitika mʼdziko lonse.

4Mudzataya dziko limene ndinakupatsani

kuti likhale cholowa chanu.

Ndidzakusandutsani akapolo otumikira adani anu

mʼdziko limene inu simukulidziwa,

chifukwa mwabutsa mkwiyo wanga ngati moto,

ndipo udzayaka mpaka muyaya.”

5Yehova akuti,

“Ndi wotembereredwa munthu amene amadalira munthu mnzake,

amene amatsamira pa munthu mnzake kuti amuthandize

pamene mtima wake wafulatira Yehova.

6Munthuyo adzakhala ngati chitsamba mʼchipululu;

iye sadzapeza zabwino.

Adzakhala mʼchipululu mopanda madzi,

mʼdziko lamchere limene munthu sangathe kukhalamo.

7“Koma ndi wodala munthu amene amadalira Yehova,

amene amatsamira pa Iye.

8Adzakhala ngati mtengo wodzalidwa mʼmphepete mwa madzi

umene umatambalitsa mizu yake mʼmbali mwa mtsinje.

Mtengowo suopa pamene kukutentha;

masamba ake amakhala obiriwira nthawi zonse.

Suchita mantha pa chaka cha chilala

ndipo sulephera kubereka chipatso.”

9Mtima wa munthu ndi wonyenga kupambana zinthu zonse

ndipo kuyipa kwake nʼkosachizika.

Ndani angathe kuwumvetsa?

10“Ine Yehova ndimafufuza mtima

ndi kuyesa maganizo,

ndimachitira munthu aliyense molingana ndi makhalidwe ake

ndiponso moyenera ntchito zake.”

11Munthu amene amapeza chuma mwachinyengo

ali ngati nkhwali imene imafungatira mazira amene sinayikire.

Pamene ali pakatikati pa moyo wake, chumacho chidzamuthera,

ndipo potsiriza adzasanduka chitsiru.

12Nyumba yathu yopemphereramo ili ngati mpando waufumu waulemerero

wokhazikitsidwa pa phiri lalitali chiyambire.

13Inu Yehova, chiyembekezo cha Israeli,

onse amene amakusiyani adzachita manyazi.

Iwo amene amakufulatirani mayina awo adzafafanizika ngati olembedwa pa fumbi

chifukwa anakana Yehova,

kasupe wa madzi amoyo.

14Inu Yehova, chiritseni, ndipo ndidzachira;

pulumutseni ndipo ndidzapulumuka,

chifukwa ndinu amene ndimakutamandani.

15Anthu akumandinena kuti,

“Mawu a Yehova ali kuti?

Zichitiketu lero kuti tizione!”

16Ine sindinakuwumirizeni kuti muwalange.

Mukudziwa kuti ine sindilakalaka tsiku la tsoka.

Zonse zimene ndinayankhula Inu mukuzidziwa.

17Musandichititse mantha;

ndinu pothawira panga pa tsiku la mavuto.

18Ondizunza anga achite manyazi,

koma musandichititse manyazi;

iwo achite mantha kwambiri,

koma ine mundichotsere manthawo.

Tsiku la mavuto liwafikire;

ndipo muwawononge kotheratu.

Kusunga Tsiku la Sabata

19Yehova anandiwuza kuti, “Pita ukayime pa chipata chodzerapo anthu, chimene mafumu a ku Yuda amalowerapo ndi kutulukirapo. Ukayimenso pa zipata zina zonse za Yerusalemu.

20Ukawawuze kuti, ‘Imvani mawu a Yehova, inu mafumu onse a ku Yuda ndi anthu onse a ku Yuda ndi inu nonse okhala mu Yerusalemu amene mumatulukira pa zipata izi.’

21Yehova akuti: samalani kuti pa tsiku la Sabata musanyamule katundu kapena kulowa naye pa zipata za Yerusalemu.

22Musalowetse katundu mʼnyumba zanu kapena kugwira ntchito pa tsiku la Sabata, koma mulipatule tsiku la Sabatalo, monga ndinalamulira makolo anu.

23Komatu iwo sanandimvere kapena kulabadira. Ndi mitima yawo yowumayo sanamvere kapena kulandira malangizo anga.

24Yehova akuti, ‘Muzimvera Ine ndi kuleka kulowetsa kapena kutulutsa katundu pa zipata za mzinda pa tsiku la Sabata. Muzisunga tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika posachita ntchito iliyonse pa tsikuli.

25Mukatero ndiye mafumu anu amene akukhala pa mpando wa Davide adzatulukira pa zipata za mzindawu pamodzi ndi nduna zawo. Iwo pamodzi ndi nduna zawo azidzalowa atakwera magaleta ndi akavalo, akuperekezedwa ndi anthu a ku Yuda ndi amene amakhala mu Yerusalemu, ndipo mu mzinda muno mudzakhala anthu mpaka muyaya.

26Anthu adzabwera kuchokera ku mizinda ya Yuda ndi ku midzi yozungulira Yerusalemu, kuchokera ku dziko la Benjamini ndi ku mapiri a kumadzulo, kuchokera ku dziko la mapiri ndi ku Negevi. Adzabwera ndi nsembe zopsereza, nsembe zaufa ndi za chakudya, nsembe za lubani ndi zopereka zachiyamiko ku nyumba ya Yehova.

27Koma ngati simundimvera; mukapanda kusunga tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika ndi kumanyamula katundu nʼkumalowa naye pa zipata za Yerusalemu pa tsikuli, Ine ndidzabutsa moto pa zipata za Yerusalemu. Moto umenewo udzanyeketsa nyumba zaufumu za ku Yerusalemu ndipo moto wake sudzazima.’ ”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help