Masalimo 43 - The Word of God in Contemporary Chichewa

Salimo 43

1Onetsani kusalakwa kwanga Inu Mulungu;

ndipo mundinenere mlandu wanga kutsutsana ndi mtundu wosapembedza;

mundilanditse mʼmanja mwa achinyengo ndi anthu oyipa.

2Pajatu Inu Mulungu ndinu mphamvu zanga.

Nʼchifukwa chiyani mwandikana ine?

Nʼchifukwa chiyani ndiyenera kuyenda ndikulira,

woponderezedwa ndi mdani?

3Tumizani kuwunika kwanu ndi choonadi chanu

kuti zinditsogolere;

mulole kuti zindifikitse ku phiri lanu loyera,

kumalo kumene inu mumakhala.

4Ndipo ndidzapita ku guwa lansembe la Mulungu,

kwa Mulungu, chimwemwe changa ndi chikondwerero changa.

Ndidzakutamandani ndi zeze,

Inu Mulungu wanga.

5Nʼchifukwa chiyani uli ndi chisoni iwe moyo wanga?

Nʼchifukwa chiyani wakhumudwa iwe mʼkati mwanga?

Khulupirira Mulungu,

pakuti ndidzamutamandabe Iye,

Mpulumutsi wanga ndi Mulungu wanga.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help