Masalimo 3 - The Word of God in Contemporary Chichewa

Salimo 3Salimo la Davide. Atathawa mwana wake Abisalomu.

1Inu Yehova, achulukadi adani anga!

Achulukadi amene andiwukira!

2Ambiri akunena za ine kuti,

“Mulungu sadzamupulumutsa.”

Sela

3Koma Inu Yehova, ndinu chishango chonditeteza,

Inu mwandiveka ulemerero ndipo mwanditukula.

4Kwa Yehova, Ine ndilira mofuwula

ndipo Iye amandiyankha kuchokera ku phiri lake loyera.

Sela

5Ine ndimagona ndi kupeza tulo;

ndimadzukanso chifukwa Yehova amandichirikiza.

6Sindidzaopa adani anga osawerengeka amene

abwera kulimbana nane kuchokera ku madera onse.

7Dzukani, Inu Yehova!

Pulumutseni, Inu Mulungu wanga.

Akantheni adani anga onse pa msagwada;

gululani mano a anthu oyipa.

8Chipulumutso chimachokera kwa Yehova.

Madalitso akhale pa anthu anu.

Sela

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help