Masalimo 122 - The Word of God in Contemporary Chichewa

Salimo 122Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

1Ndinakondwera atandiwuza kuti,

“Tiyeni ku nyumba ya Yehova.”

2Mapazi athu akuyima mʼzipata

zako, Iwe Yerusalemu.

3Yerusalemu anamangidwa ngati mzinda

umene uli wothithikana pamodzi.

4Kumeneko ndiye kumene kumapita mafuko,

mafuko a Yehova,

umboni wa kwa Israeli,

kuti atamande dzina la Yehova.

5Kumeneko anayikako mipando yaufumu yachiweruzo,

mipando yaufumu ya nyumba ya Davide.

6Pemphererani mtendere wa Yerusalemu:

“Iwo amene amakukonda iwe zinthu ziwayendere bwino.

7Mukhale mtendere mʼkati mwa makoma ako,

ndipo mʼnyumba zako zaufumu mukhale chitetezo.”

8Chifukwa cha abale anga ndi abwenzi anga

ndidzati, “Mtendere ukhale mʼkati mwako.”

9Chifukwa cha Nyumba ya Yehova Mulungu wathu,

ndidzakufunira zabwino.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help