Yobu 25 - The Word of God in Contemporary Chichewa

Mawu a Bilidadi

1Apo Bilidadi wa ku Suki anayankha kuti,

2“Ulamuliro ndi kuopsa ndi za Mulungu,

Iye amakhazikitsa bata mu ufumu wake kumwambako.

3Kodi magulu ake ankhondo nʼkuwerengeka?

Kodi kuwala kwake sikuwalira ndani?

4Kodi munthu angakhale bwanji wolungama pamaso pa Mulungu?

Kodi munthu wobadwa mwa mayi angakhale wangwiro?

5Ngati mwezi sutha kuwala kwenikweni,

ndipo nyenyezi sizitha kuwala pamaso pake,

6nanji tsono munthu amene ali ngati mphutsi,

mwana wa munthu amene ali ngati nyongolotsi!”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help