Masalimo 98 - The Word of God in Contemporary Chichewa

Salimo 98Salimo.

1Imbirani Yehova nyimbo yatsopano,

pakuti Iyeyo wachita zinthu zodabwitsa;

dzanja lake lamanja ndi mkono wake woyera

zamuchitira chipulumutso.

2Yehova waonetsa chipulumutso chake

ndipo waulula chilungamo chake kwa anthu a mitundu ina.

3Iye wakumbukira chikondi chake

ndi kukhulupirika kwake pa Aisraeli;

malekezero onse a dziko lapansi aona

chipulumutso cha Mulungu wathu.

4Fuwulani mwachimwemwe kwa Yehova, dziko lonse lapansi,

muyimbireni nyimbo mofuwula ndi mokondwera.

5Imbirani Yehova nyimbo ndi zeze,

ndi zeze ndi mawu a kuyimba,

6ndi malipenga ndi kuliza kwa nyanga ya nkhosa yayimuna

fuwulani mwachimwemwe pamaso pa Yehova Mfumu.

7Nyanja ikokome pamodzi ndi zonse zili mʼmenemo,

dziko lonse ndi onse amene amakhala mʼmenemo.

8Mitsinje iwombe mʼmanja mwawo,

mapiri ayimbe pamodzi mwachimwemwe;

9izo ziyimbe pamaso pa Yehova,

pakuti Iye akubwera kudzaweruza dziko lapansi.

Adzaweruza dziko lonse mwachilungamo,

ndi mitundu ya anthu mosakondera.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help