Masalimo 142 - The Word of God in Contemporary Chichewa

Salimo 142Ndakatulo ya Davide, pamene iyeyo anali mʼphanga. Pemphero.

1Ndikulirira Yehova mofuwula;

ndikukweza mawu anga kwa Yehova kupempha chifundo.

2Ndikukhuthula madandawulo anga pamaso pake;

ndikufotokoza za masautso anga pamaso pake.

3Pamene mzimu wanga walefuka mʼkati mwanga,

ndinu amene mudziwa njira yanga.

Mʼnjira imene ndimayendamo

anthu anditchera msampha mobisa.

4Yangʼanani kumanja kwanga ndipo onani;

palibe amene akukhudzika nane.

Ndilibe pothawira;

palibe amene amasamala za moyo wanga.

5Ndilirira Inu Yehova;

ndikuti, “Ndinu pothawirapo panga,

gawo langa mʼdziko la anthu amoyo.”

6Mverani kulira kwanga

pakuti ndathedwa nzeru;

pulumutseni kwa amene akundithamangitsa

pakuti ndi amphamvu kuposa ine.

7Tulutseni mʼndende yanga

kuti nditamande dzina lanu.

Ndipo anthu olungama adzandizungulira

chifukwa cha zabwino zanu pa ine.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help