Masalimo 147 - The Word of God in Contemporary Chichewa

Salimo 147

1Tamandani Yehova.

Nʼkwabwino kwambiri kuyimba nyimbo zamatamando kwa Mulungu wathu,

nʼkokondweretsa ndi koyenera kumutamanda!

2Yehova akumanga Yerusalemu;

Iye akusonkhanitsa amʼndende a Israeli.

3Akutsogolera anthu osweka mtima

ndi kumanga mabala awo.

4Amadziwa chiwerengero cha nyenyezi,

ndipo iliyonse amayitchula dzina.

5Yehova ndi wamkulu ndi wamphamvu kwambiri;

nzeru zake zilibe malire.

6Yehova amagwiriziza anthu odzichepetsa,

koma amagwetsa pansi anthu oyipa.

7Imbirani Yehova ndi mayamiko;

imbani nyimbo kwa Mulungu ndi pangwe.

8Iye amaphimba mlengalenga ndi mitambo;

amapereka mvula ku dziko lapansi

ndi kumeretsa udzu mʼmapiri.

9Iye amapereka chakudya kwa ngʼombe

ndi kwa ana a makwangwala pamene akulira chakudya.

10Chikondwerero chake sichili mʼmphamvu za kavalo,

kapena mʼmiyendo ya anthu amphamvu.

11Yehova amakondwera ndi amene amamuopa,

amene chiyembekezo chawo chili mʼchikondi chake chosasinthika.

12Lemekeza Yehova, iwe Yerusalemu;

tamanda Mulungu wako, iwe Ziyoni,

13pakuti Iye amalimbitsa mipiringidzo ya zipata zako

ndi kudalitsa anthu ako mwa iwe.

14Iye amabweretsa mtendere mʼmalire mwako

ndi kukukhutitsa ndi ufa wa tirigu wosalala.

15Iyeyo amapereka lamulo pa dziko lapansi;

mawu ake amayenda mwaliwiro.

16Amagwetsa chisanu ngati ubweya

ndi kumwaza chipale ngati phulusa.

17Amagwetsa matalala ngati miyala.

Kodi ndani angathe kupirira kuzizira kwake?

18Amatumiza mawu ake ndipo chisanucho chimasungunuka;

amawombetsa mphepo ndipo madzi amayenda.

19Iye anawulula mawu ake kwa Yakobo,

malamulo ake ndi zophunzitsa zake kwa Israeli.

20Sanachitepo zimenezi kwa mtundu wina uliwonse wa anthu;

anthu enawo sadziwa malamulo ake.

Tamandani Yehova.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help