1Uthenga wonena za Mowabu:
Popeza kuti mu usiku umodzi wokha mzinda wa Ari wa ku Mowabu wawonongedwa,
wawonongedwa pa usiku umodzi wokha.
Mzinda wa Kiri wawonongedwa,
wawonongedwa pa usiku umodzi wokha.
2Anthu a ku Diboni akupita ku nyumba ya milungu yawo,
akupita ku malo awo achipembedzo kukalira;
anthu a ku Mowabu akulirira mofuwula mzinda wa Nebo ndi wa Medeba.
Mutu uliwonse wametedwa mpala,
ndipo ndevu zonse zametedwa.
3Mʼmisewu akuvala ziguduli;
pa madenga ndi mʼmabwalo
aliyense akulira mofuwula,
misozi ili pupupu.
4Anthu a ku Hesiboni ndi Eleali akulira mofuwula,
mawu awo akumveka mpaka ku Yahazi.
Kotero asilikali a ku Mowabu akulira mofuwula,
ndipo ataya mtima.
5Inenso ndikulirira Mowabu;
chifukwa othawa nkhondo ake akupita akulira ku chikweza cha Luluti mpaka ku Zowari
ndi Egilati-Selisiya
akupita akulira ku chikweza cha Luhiti,
Akulira mosweka mtima
pa njira yopita ku Horonaimu;
akulira mosweka mtima chifukwa cha chiwonongeko chawo.
6Madzi a ku Nimurimu aphwa
ndipo udzu wauma;
zomera zawonongeka
ndipo palibe chomera chobiriwira chatsala.
7Kotero kuti chuma chomwe anachipeza ndi kuchisunga,
achitenga kuti awoloke nacho chigwembe cha Misondozi.
8Kulira kwawo kukumveka mʼdziko lonse la Mowabu;
kulira kwawo kosweka mtima kukumveka
mpaka ku Egilaimu ndi Beeri-Elimu.
9Madzi a ku Dimoni afiira ndi magazi,
komabe ndidzabweretsa zina zambiri pa Dimoni,
mkango woti udzagwire aliyense othawa mu Mowabu
ndi aliyense wotsala mʼdzikomo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.