1Inu Yehova, mtima wanga siwodzikuza,
maso anga siwonyada;
sinditengeteka mtima
ndi zinthu zapamwamba ndi zodabwitsa.
2Koma moyo wanga ndawutontholetsa
ndi kuwukhalitsa chete ngati mwana amene amayi ake amuletsa kuyamwa,
moyo wanga mʼkati mwanga uli ngati mwana amene amuletsa kuyamwa.
3Yembekeza Yehova, iwe Israeli,
kuyambira tsopano mpaka muyaya.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.